-
Yeremiya 7:23, 24Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
23 Koma ndinawalamula kuti: “Muzimvera mawu anga, ndipo ndidzakhala Mulungu wanu, inuyo mudzakhala anthu anga.+ Muziyenda mʼnjira imene ndakulamulani, kuti zinthu zikuyendereni bwino.”’+ 24 Koma iwo sanamvere kapena kutchera khutu.+ Mʼmalomwake, anayenda motsatira zofuna zawo. Mouma khosi anatsatira zofuna za mtima wawo woipawo,+ moti anabwerera mʼmbuyo mʼmalo mopita patsogolo,
-
-
Yeremiya 11:7, 8Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
7 Inetu ndinkalangiza makolo anu pa tsiku limene ndinawatulutsa mʼdziko la Iguputo ndipo ndikupitiriza mpaka pano. Ndinkawalangiza mobwerezabwereza* kuti: “Muzimvera mawu anga.”+ 8 Koma iwo sanamvere kapena kutchera khutu. Mʼmalomwake aliyense wa iwo anapitiriza kuumitsa mtima wake ndi kuchita zofuna za mtima wake woipawo.+ Choncho ndinawalanga mogwirizana ndi mawu onse a mʼpangano langa limene ndinawalamula kuti azilitsatira koma iwo anakana kulitsatira.’”
-