-
Ekisodo 1:8-10Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
8 Patapita nthawi, mfumu ina yomwe sinkamudziwa Yosefe inayamba kulamulira ku Iguputo. 9 Mfumuyo inauza anthu ake kuti: “Taonani! Aisiraeli achuluka kwambiri ndipo ndi amphamvu kuposa ife.+ 10 Tiyeni tiwachenjerere anthu amenewa kuti asapitirize kuchulukana, kuopera kuti pa nthawi ya nkhondo angadzagwirizane ndi adani athu nʼkumenyana nafe kenako nʼkuchoka mʼdziko muno.”
-
-
Esitere 3:6Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
6 Koma Hamani anaona kuti nʼzosakwanira kupha Moredikayi yekha chifukwa anthu anali atamuuza za anthu a mtundu wa Moredikayi. Choncho Hamani anaganiza zoti aphe Ayuda onse, anthu a mtundu wa Moredikayi mʼmadera onse amene Ahasiwero ankalamulira.
-