25 Anagwiranso akalonga awiri a Amidiyani, Orebi ndi Zeebi. Atatero, anapha Orebi pathanthwe la Orebi,+ ndipo Zeebi anamuphera pamalo opondera mphesa a Zeebi. Iwo anapitiriza kuthamangitsa Amidiyani+ ndipo anabweretsa mutu wa Orebi ndi wa Zeebi kwa Gidiyoni mʼchigawo cha Yorodano.