21 Choncho Zeba ndi Zalimuna anati: “Nyamuka iweyo utiphe wekha. Munthu amaweruzidwa mogwirizana ndi mphamvu zake.” Ndiyeno Gidiyoni ananyamuka nʼkupha Zeba ndi Zalimuna,+ ndipo anatenga zokongoletsa zooneka ngati mwezi zimene zinali pamakosi a ngamila zawo.