3 Ndi ndani angakwere kuphiri la Yehova,+
Ndipo ndi ndani angaime mʼmalo ake opatulika?
4 Aliyense amene ndi wosalakwa komanso wopanda chinyengo mumtima mwake,+
Amene sanalumbire mwachinyengo potchula moyo Wanga,
Kapena kulumbira pofuna kupusitsa anthu ena.+