26 Kenako Sauli anafika mbali ina ya phiri limene Davide ndi amuna amene anali naye anabisala. Zitatero Davide anayamba kukonzeka mwamsanga kuti athawe+ Sauli. Pa nthawiyi nʼkuti Sauli ndi asilikali ake atatsala pangʼono kupeza Davide ndi amuna amene anali naye.+