Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Deuteronomo 4:6
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 6 Muzitsatira malangizo ndi zigamulo zimenezi mosamala kwambiri,+ chifukwa mukachita zimenezi mudzasonyeza kuti ndinu anzeru+ komanso ozindikira+ pamaso pa anthu a mitundu ina amene adzamva za malangizo onsewa ndipo adzanena kuti, ‘Mtundu waukulu umenewu ndi wa anthu anzerudi komanso ozindikira.’+

  • Yoswa 1:7, 8
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 7 Ukhale wolimba mtima kwambiri ndipo uchite zinthu mwamphamvu. Uonetsetse kuti ukutsatira malamulo onse amene mtumiki wanga Mose anakulamula. Usapatukire kudzanja lamanja kapena lamanzere,+ kuti uzichita zinthu mwanzeru kulikonse kumene ungapite.+ 8 Buku la Chilamulo ili lisachoke pakamwa pako.+ Uziliwerenga ndi kuganizira mozama* masana ndi usiku, kuti uzitsatira bwinobwino zonse zimene zalembedwamo.+ Ukamatero, zizikuyendera bwino ndipo uzichita zinthu mwanzeru.+

  • 1 Mafumu 2:3
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 3 Uzimvera Yehova Mulungu wako poyenda mʼnjira zake komanso posunga malamulo ake, ziweruzo zake ndiponso zikumbutso zake mogwirizana ndi mmene anazilembera mʼChilamulo cha Mose.+ Ukatero zinthu zidzakuyendera bwino* pa zonse zimene ungachite ndiponso kulikonse kumene ungapite.

  • Salimo 119:100
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 100 Ndimachita zinthu mozindikira kuposa anthu achikulire,

      Chifukwa ndimatsatira malamulo anu.

  • 2 Timoteyo 3:14, 15
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 14 Koma iwe, pitiriza kutsatira zimene unaphunzira ndi zimene unakhulupirira pambuyo pokhutira nazo,+ chifukwa ukudziwa amene anakuphunzitsa. 15 Kuyambira pamene unali wakhanda,+ wadziwa malemba oyera+ amene angakupatse nzeru zokuthandiza kuti udzapulumuke chifukwa chokhulupirira Khristu Yesu.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena