-
Aheberi 12:9-11Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
9 Bambo athu otibereka ankatilanga ndipo tinkawalemekeza. Ndiye kuli bwanji Atate wa moyo wathu wauzimu? Kodi sitiyenera kuwagonjera koposa pamenepo kuti tikhale ndi moyo?+ 10 Chifukwa bambo athu otiberekawo, anatilanga kwa nthawi yochepa mogwirizana ndi zimene ankaziona kuti nʼzoyenera, koma Mulungu amatilanga kuti zinthu zitiyendere bwino ndiponso kuti tikhale oyera ngati iyeyo.+ 11 Nʼzoona kuti palibe chilango chimene chimakhala chosangalatsa pa nthawi yomwe ukuchilandira, koma chimakhala chowawa. Komabe pambuyo pake, kwa anthu amene aphunzirapo kanthu pa chilangocho, chimabala chipatso chamtendere, chomwe ndi chilungamo.
-