Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • 2 Samueli 22:26-31
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 26 Munthu wokhulupirika, mumamuchitira mokhulupirika.+

      Munthu wamphamvu komanso wosalakwa, mumamuchitira mwachilungamo.+

      27 Munthu woyera, mumamusonyeza kuti ndinu woyera,+

      Koma munthu wamaganizo opotoka mumamusonyeza kuti ndinu wochenjera.+

      28 Mumapulumutsa anthu odzichepetsa,+

      Koma mumanyansidwa ndi anthu odzikweza ndipo mumawatsitsa.+

      29 Inu Yehova ndinu nyale yanga;+

      Yehova ndi amene amandiunikira mumdima.+

      30 Ndi thandizo lanu ndingalimbane ndi gulu la achifwamba;

      Ndi mphamvu za Mulungu ndingakwere khoma.+

      31 Njira ya Mulungu woona ndi yangwiro.+

      Mawu a Yehova ndi oyengeka bwino.+

      Iye ndi chishango kwa onse othawira kwa iye.+

  • Yobu 34:11
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 11 Chifukwa iye amapereka mphoto kwa munthu mogwirizana ndi zimene amachita,+

      Ndipo amamusiya kuti akumane ndi mavuto chifukwa cha zochita zake.

  • Yeremiya 32:19
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 19 Zolinga zanu ndi zazikulu ndipo zochita zanu ndi zamphamvu.+ Maso anu amaona zonse zimene anthu amachita,+ kuti munthu aliyense mumuchitire zinthu mogwirizana ndi njira zake komanso zochita zake.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena