-
1 Samueli 23:26-28Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
26 Kenako Sauli anafika mbali ina ya phiri limene Davide ndi amuna amene anali naye anabisala. Zitatero Davide anayamba kukonzeka mwamsanga kuti athawe+ Sauli. Pa nthawiyi nʼkuti Sauli ndi asilikali ake atatsala pangʼono kupeza Davide ndi amuna amene anali naye.+ 27 Koma kenako kunabwera munthu ndi uthenga wakuti: “Bwerani mofulumira, Afilisiti aukira dziko lathu!” 28 Zitatero Sauli anasiya kusakasaka Davide+ ndipo anabwerera kukamenyana ndi Afilisiti. Nʼchifukwa chake malowo anawapatsa dzina lakuti Thanthwe Logawanitsa.
-
-
2 Samueli 17:21, 22Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
21 Anthuwo atachoka, Ahimazi ndi Yonatani anatuluka mʼchitsimemo nʼkupita kukauza Mfumu Davide kuti: “Nyamukani mwamsanga ndipo muwoloke mtsinje.” Kenako anawauza malangizo amene Ahitofeli anapereka.+ 22 Nthawi yomweyo Davide ananyamuka pamodzi ndi anthu onse amene anali naye, ndipo anawoloka Yorodano. Pofika mʼbandakucha, aliyense anali atawoloka Yorodano.
-