Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Nehemiya 4:4
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 4 Nehemiya anati: “Inu Mulungu wathu, onani mmene akutinyozera.+ Abwezereni chipongwe chawo+ ndipo lolani kuti atengedwe ngati katundu kupita ku ukapolo.

  • Nehemiya 6:15, 16
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 15 Choncho ntchito yomanga mpanda inatha pa tsiku la 25 la mwezi wa Eluli* ndipo inatenga masiku 52.

      16 Adani athu onse atangomva zimenezi komanso anthu a mitundu ina yotizungulira ataona, anachita manyazi kwambiri+ ndipo anazindikira kuti ntchitoyi yatheka chifukwa cha Mulungu wathu.

  • Esitere 6:13
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 13 Hamani atafotokozera mkazi wake Zeresi+ ndiponso anzake onse zonse zimene zinamuchitikira, amuna anzeru amene ankamutumikira komanso mkazi wakeyo anati: “Ngati wayamba kufooka pamaso pa Moredikayi, yemwe ndi Myuda, ndiye kuti supambana koma akugonjetsa ndithu.”

  • Esitere 9:5
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 5 Ndiyeno Ayuda anapha adani awo onse ndi lupanga. Ayudawo anachita zonse zimene ankafuna kwa adani awo.+

  • Salimo 137:7
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    •  7 Inu Yehova, kumbukirani

      Zimene Aedomu ananena pa tsiku limene Yerusalemu anawonongedwa.

      Iwo anati: “Gwetsani mzindawo! Ugwetseni mpaka pamaziko ake!”+

  • Zekariya 12:3
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 3 Pa tsiku limenelo, Yerusalemu ndidzamusandutsa mwala wolemera* kwa anthu a mitundu yonse. Onse onyamula mwala umenewo, adzavulala koopsa.+ Anthu a mitundu yonse yapadziko lapansi adzasonkhana kuti amuukire.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena