1 Samueli 3:3 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 3 Nyale ya Mulungu+ inali isanazimitsidwe, ndipo Samueli anali atagona mʼkachisi*+ wa Yehova mmene munali Likasa la Mulungu. 1 Mbiri 16:1 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 16 Choncho anabweretsa Likasa la Mulungu woona pamalo amene Davide anakonza nʼkuliika mutenti imene iye anamanga kuti lizikhalamo.+ Kenako iwo anapereka nsembe zopsereza ndi nsembe zamgwirizano kwa Mulungu woona.+ Salimo 27:4 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 4 Ndapempha chinthu chimodzi kwa Yehova,Chimenecho ndi chimene ndikuchilakalaka.Chinthu chake nʼchakuti, ndikhale mʼnyumba ya Yehova masiku onse a moyo wanga,+Kuti ndione ubwino wa Yehova,Komanso kuti ndiyangʼane kachisi wake* moyamikira.*+
3 Nyale ya Mulungu+ inali isanazimitsidwe, ndipo Samueli anali atagona mʼkachisi*+ wa Yehova mmene munali Likasa la Mulungu.
16 Choncho anabweretsa Likasa la Mulungu woona pamalo amene Davide anakonza nʼkuliika mutenti imene iye anamanga kuti lizikhalamo.+ Kenako iwo anapereka nsembe zopsereza ndi nsembe zamgwirizano kwa Mulungu woona.+
4 Ndapempha chinthu chimodzi kwa Yehova,Chimenecho ndi chimene ndikuchilakalaka.Chinthu chake nʼchakuti, ndikhale mʼnyumba ya Yehova masiku onse a moyo wanga,+Kuti ndione ubwino wa Yehova,Komanso kuti ndiyangʼane kachisi wake* moyamikira.*+