Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Salimo 49:10
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 10 Aliyense amaona kuti ngakhale anthu anzeru amafa,

      Munthu wopusa komanso munthu wopanda nzeru, onse amawonongeka,+

      Ndipo chuma chawo amasiyira anthu ena.+

  • Mlaliki 2:18, 19
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 18 Ndinayamba kudana ndi zinthu zonse zimene ndinapeza nditagwira ntchito mwakhama padziko lapansi pano,+ chifukwa ndidzayenera kusiyira munthu amene akubwera pambuyo panga.+ 19 Ndipo ndi ndani akudziwa ngati angadzakhale wanzeru kapena wopusa?+ Koma adzatenga zinthu zanga zonse zimene ndinapeza nditagwira ntchito mwakhama komanso mwanzeru padziko lapansi pano. Zimenezinso nʼzachabechabe.

  • Mlaliki 4:8
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 8 Pali munthu amene ali yekhayekha, wopanda mnzake. Alibe mwana kapena mchimwene wake, koma amangokhalira kugwira ntchito mwakhama. Maso ake sakhutira ndi chuma.+ Koma kodi amadzifunsa kuti, “Ndikamagwira ntchito mwakhama komanso kudzimana zinthu zabwino, kodi ndikufuna kuti zinthu zimenezi adzasangalale nazo ndani?”+ Izinso nʼzachabechabe ndipo ndi ntchito yobweretsa nkhawa.+

  • Luka 12:19, 20
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 19 ndiye ndidzadziuza kuti: “Uli ndi zinthu zambiri zabwino ndipo zisungika kwa zaka zambiri. Mtima mʼmalo, udye, umwe ndi kusangalala.”’ 20 Koma Mulungu anamuuza kuti, ‘Wopanda nzeru iwe, usiku womwe uno moyo wako aufuna. Nanga zinthu zimene wasungazi zidzakhala za ndani?’+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena