-
Aheberi 10:5-9Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
5 Choncho atabwera padzikoli iye anati: “‘Nsembe zanyama komanso nsembe zina simunazifune, koma munandikonzera thupi. 6 Nsembe zopsereza zathunthu ndi nsembe zamachimo simunazivomereze.’+ 7 Ndiyeno ine ndinati, ‘Taonani! Ine ndabwera (mumpukutu munalembedwa za ine) kudzachita chifuniro chanu, inu Mulungu wanga.’”+ 8 Atanena kuti: “Nsembe zanyama, nsembe zopsereza zathunthu, nsembe zamachimo ndiponso nsembe zina simunazifune kapena kuzivomereza,” zomwe ndi nsembe zoperekedwa mogwirizana ndi Chilamulo. 9 Ananenanso kuti: “Taonani! Ine ndabwera kudzachita chifuniro chanu.”+ Akuchotsa dongosolo loyambalo kuti akhazikitse lachiwiri.
-