-
Machitidwe 4:25-28Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
25 Pogwiritsa ntchito mzimu woyera, inu munanena kudzera pakamwa pa kholo lathu Davide+ mtumiki wanu kuti, ‘Nʼchifukwa chiyani anthu a mitundu ina akuchita chipolowe ndiponso nʼchifukwa chiyani mitundu ya anthu ikuganizira* zinthu zopanda pake? 26 Mafumu a dziko lapansi anaima pamalo awo, ndipo olamulira anasonkhana mogwirizana kuti alimbane ndi Yehova* komanso wodzozedwa* wake.’+ 27 Zimenezi zinachitikadi pamene Herode, Pontiyo Pilato,+ anthu a mitundu ina komanso anthu a mu Isiraeli, anasonkhana mumzindawu nʼkuukira Yesu, mtumiki wanu woyera, amene inu munamudzoza.+ 28 Anasonkhana kuti achite zimene munaneneratu. Zimenezi zinachitika chifukwa inu muli ndi mphamvu komanso chifukwa zinali zogwirizana ndi chifuniro chanu.+
-