-
Yeremiya 7:22, 23Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
22 Chifukwatu pa tsiku limene ndinatulutsa makolo anu mʼdziko la Iguputo, sindinalankhule nawo chilichonse kapena kuwalamula zokhudza kupereka nsembe zopsereza zathunthu ndi nsembe zina.+ 23 Koma ndinawalamula kuti: “Muzimvera mawu anga, ndipo ndidzakhala Mulungu wanu, inuyo mudzakhala anthu anga.+ Muziyenda mʼnjira imene ndakulamulani, kuti zinthu zikuyendereni bwino.”’+
-