7 Kodi Yehova adzasangalala ndi masauzande a nkhosa zamphongo?
Kodi adzakondwera ndi mitsinje ya mafuta masauzande ambirimbiri?+
Kodi ndipereke mwana wanga wamwamuna woyamba chifukwa cha zolakwa zanga,
Ndipereke chipatso cha mimba yanga chifukwa cha tchimo langa?+