-
2 Mbiri 33:12, 13Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
12 Iye atavutika kwambiri ndi zimenezi, anapempha Yehova kuti amuchitire chifundo* ndipo anadzichepetsa kwambiri pamaso pa Mulungu wa makolo ake. 13 Manase anayamba kupemphera kwa Mulungu ndipo iye anamva pemphero lake lochonderera ndiponso lopempha chifundo. Kenako anamʼbwezera ku Yerusalemu ndipo anakhalanso mfumu.+ Zitatero, Manase anadziwa kuti Yehova ndi Mulungu woona.+
-