24 Choncho, mofanana ndi mmene lawi la moto limapserezera mapesi
Komanso mmene udzu wouma umayakira mʼmalawi a moto,
Mizu yawo idzawola,
Ndipo maluwa awo adzauluzika ngati fumbi,
Chifukwa akana malamulo a Yehova wa magulu ankhondo akumwamba
Ndipo anyoza mawu a Woyera wa Isiraeli.+