Deuteronomo 6:6, 7 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 6 Mawu awa amene ndikukulamulani lerowa azikhala pamtima panu, 7 ndipo muziwakhomereza* mumtima mwa ana anu.+ Muzilankhula nawo mawuwo mukakhala pansi mʼnyumba mwanu, mukamayenda pamsewu, mukamagona komanso mukadzuka.+ Aefeso 6:4 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 4 Inu abambo, musamapsetse mtima ana anu,+ koma pitirizani kuwalera powapatsa malangizo*+ komanso kuwaphunzitsa mogwirizana ndi zimene Yehova* amanena.+ Aheberi 12:9 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 9 Bambo athu otibereka ankatilanga ndipo tinkawalemekeza. Ndiye kuli bwanji Atate wa moyo wathu wauzimu? Kodi sitiyenera kuwagonjera koposa pamenepo kuti tikhale ndi moyo?+
6 Mawu awa amene ndikukulamulani lerowa azikhala pamtima panu, 7 ndipo muziwakhomereza* mumtima mwa ana anu.+ Muzilankhula nawo mawuwo mukakhala pansi mʼnyumba mwanu, mukamayenda pamsewu, mukamagona komanso mukadzuka.+
4 Inu abambo, musamapsetse mtima ana anu,+ koma pitirizani kuwalera powapatsa malangizo*+ komanso kuwaphunzitsa mogwirizana ndi zimene Yehova* amanena.+
9 Bambo athu otibereka ankatilanga ndipo tinkawalemekeza. Ndiye kuli bwanji Atate wa moyo wathu wauzimu? Kodi sitiyenera kuwagonjera koposa pamenepo kuti tikhale ndi moyo?+