13 Waulesi amanena kuti: “Mumsewu muli mkango wamphamvu,
Mʼbwalo la mzinda mukuyendayenda mkango.”+
14 Mofanana ndi chitseko chimene chimangozungulira pamene anachimangirira,
Waulesi nayenso amangotembenukatembenuka pabedi pake.+
15 Munthu waulesi amapisa dzanja lake mʼmbale ya chakudya,
Koma amalephera kulibweretsa pakamwa pake chifukwa chotopa kwambiri.+