-
Miyambo 4:7-9Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
7 Nzeru ndi chinthu chofunika kwambiri,+ choncho upeze nzeru,
Ndipo pa zinthu zonse zimene upeze, upezenso luso lomvetsa zinthu.+
8 Uzilemekeze kwambiri ndipo zidzakukweza.+
Zidzakulemekeza chifukwa chakuti wazikumbatira.+
9 Zidzaika nkhata yamaluwa yokongola kumutu kwako.
Zidzakuveka chisoti chachifumu chokongola.”
-