-
1 Samueli 17:45, 46Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
45 Davide anayankha Mfilisitiyo kuti: “Iwe ukubwera kudzamenyana ndi ine ndi lupanga, mkondo ndi nthungo,+ koma ine ndikubwera kudzamenyana nawe mʼdzina la Yehova wa magulu ankhondo akumwamba,+ Mulungu wa asilikali a Isiraeli, amene iweyo wamunyoza.+ 46 Lero Yehova akupereka mʼmanja mwanga,+ ndipo ndikupha nʼkukudula mutu. Lero ndipereka mitembo ya asilikali amʼmisasa ya Afilisiti kwa mbalame zamumlengalenga ndi kwa zilombo zakutchire. Anthu onse apadziko lapansi adzadziwa kuti Aisiraeli ali ndi Mulungu.+
-