-
1 Mafumu 3:7-9Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
7 Tsopano Yehova Mulungu wanga, mwandiika ine mtumiki wanu kukhala mfumu mʼmalo mwa Davide bambo anga, ngakhale kuti ndine wamngʼono ndipo sindikudziwa zambiri.+ 8 Ine mtumiki wanu ndili pakati pa anthu anu amene mwawasankha,+ anthu ambirimbiri osatheka kuwawerenga. 9 Mundipatse ine mtumiki wanu mtima womvera kuti ndiweruze anthu anu+ komanso ndizitha kusiyanitsa zabwino ndi zoipa.+ Ndani angathe kuweruza anthu anu ambirimbiriwa?”*
-