14 Aisiraeli anatenga cholowa chawo mʼdziko la Kanani. Wansembe Eliezara, Yoswa mwana wa Nuni ndi atsogoleri a mafuko a makolo a Aisiraeli ndi amene anawagawira cholowachi.+ 2 Pogawa cholowacho kwa mafuko 9 ndi hafu,+ anachita maere+ mogwirizana ndi zimene Yehova analamula kudzera mwa Mose.