-
Ezekieli 26:2, 3Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
2 “Iwe mwana wa munthu, Turo wanena Yerusalemu+ kuti, ‘Eyaa! Zakhala bwino. Mzinda umene unkakopa anthu a mitundu ina wathyoledwa.+ Tsopano zinthu zindiyendera bwino ndipo ndilemera chifukwa mzindawo wawonongedwa.’ 3 Choncho Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti, ‘Ine ndikuukira iwe Turo ndipo ndikutumizira mayiko ambiri kuti adzamenyane nawe. Iwo adzabwera ngati mafunde amʼnyanja.
-