-
2 Mafumu 5:20-22Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
20 Gehazi,+ mtumiki wa Elisa munthu wa Mulungu woona,+ anaganiza mumtima mwake kuti: ‘Zoona mbuyanga wangomusiya Namani wa ku Siriya+ uja osalandira zinthu zomwe anabweretsa? Ndikulumbira mʼdzina la Yehova Mulungu wamoyo, ndimʼthamangira kuti ndikatengeko zinthu zina.’ 21 Gehazi anathamangiradi Namani ndipo Namani ataona kuti munthu akumʼthamangira, anatsika pagaleta lake kuti akumane naye. Kenako anati: “Nʼkwabwino?” 22 Gehazi anayankha kuti: “Inde nʼkwabwino. Mbuyanga wandituma kuti, ‘Posachedwapa kwabwera anyamata awiri, ana a aneneri, kuchokera kudera lamapiri la Efuraimu. Muwapatseko talente imodzi ya siliva ndi zovala ziwiri.’”+
-