-
1 Samueli 18:8, 9Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
8 Sauli anakwiya kwambiri+ ndipo nyimbo imeneyi inkamunyasa, moti anayamba kuganiza kuti: “Akutamanda Davide ponena kuti wapha masauzande ambirimbiri, koma ine akunena kuti ndapha masauzande okha. Ndiye kuti kwatsala nʼkumupatsa ufumuwutu basi!”+ 9 Kuyambira tsiku limenelo, Sauli anayamba kuyangʼana Davide ndi diso loipa.
-