-
1 Samueli 8:1-3Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
8 Samueli atakalamba, anaika ana ake aamuna kuti akhale oweruza mu Isiraeli. 2 Mwana wake woyamba anali Yoweli, ndipo wachiwiri anali Abiya.+ Iwo anali oweruza ku Beere-seba. 3 Ana akewa sanatsatire chitsanzo chake. Iwo ankakonda kupeza phindu mwachinyengo,+ kulandira ziphuphu+ ndiponso kupotoza chilungamo.+
-