26 Kenako Mulungu anati: “Tiyeni+ tipange munthu mʼchifaniziro+ chathu, kuti akhale wofanana nafe.+ Ayangʼanire nsomba zamʼnyanja, zamoyo zouluka mumlengalenga, nyama zoweta ndiponso nyama iliyonse yokwawa padziko lapansi. Komanso asamalire dziko lonse lapansi.”+