25 Mumtima mwanga ndinasankha kuti ndidziwe, ndifufuze ndiponso ndifunefune nzeru komanso chifukwa chake zinthu zinazake zimachitika. Ndinafunanso kumvetsa kuti uchitsiru ndi woipa bwanji komanso makhalidwe opusa a anthu amene amachita zinthu ngati amisala.+