13 Golide amene ankabwera kwa Solomo pa chaka, anali wolemera matalente 666,+ 14 osawerengera golide wochokera kwa amalonda oyendayenda ndi amalonda ena, komanso wochokera kwa mafumu onse a Aluya ndi kwa abwanamkubwa amʼdzikolo, amene ankabweretsa golide ndi siliva kwa Solomo.+