9 Mnyamata iwe, sangalala pa nthawi imene uli wachinyamata, ndipo mtima wako usangalale masiku a unyamata wako. Uzichita zimene mtima wako ukufuna ndipo uzipita kumene maso ako akukutsogolera. Koma dziwa kuti Mulungu woona adzakuweruza pa zinthu zonsezi.+