-
1 Samueli 13:12, 13Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
12 Ndiye ndinaganiza kuti, ‘Afilisitiwa abwera ku Giligala kuno kudzamenyana nane, ndipo sindinakhazike pansi mtima wa Yehova.’ Choncho ndinaona kuti ndiyenera kupereka nsembe yopsereza.”
13 Koma Samueli anauza Sauli kuti: “Zimene wachitazi ndi zopusa. Sunamvere lamulo limene Yehova Mulungu wako anakupatsa.+ Ukanamvera, Yehova akanachititsa kuti banja lako lilamulire Isiraeli mpaka kalekale.
-