-
Luka 12:18-20Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
18 Ndiyeno anati, ‘Ndichita izi:+ Ndigwetsa nyumba zanga zosungiramo zinthu nʼkumanga zikuluzikulu, ndipo tirigu wanga yense ndi zinthu zanga zonse ndidzazitutira mmenemo, 19 ndiye ndidzadziuza kuti: “Uli ndi zinthu zambiri zabwino ndipo zisungika kwa zaka zambiri. Mtima mʼmalo, udye, umwe ndi kusangalala.”’ 20 Koma Mulungu anamuuza kuti, ‘Wopanda nzeru iwe, usiku womwe uno moyo wako aufuna. Nanga zinthu zimene wasungazi zidzakhala za ndani?’+
-