Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Ekisodo 30:23
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 23 “Kenako utenge mafuta onunkhira, abwino kwambiri awa: mule* woundana wokwana masekeli 500, sinamoni wonunkhira bwino hafu ya muyezo wa mule, kapena kuti masekeli 250, ndi kalamasi wonunkhira wokwana masekeli 250.

  • Ekisodo 30:25
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 25 Zinthu zimenezi upangire mafuta ogwiritsa ntchito pa kudzoza kopatulika, mafuta onunkhira osakanizidwa mwaluso.*+ Akhale mafuta ogwiritsa ntchito pa kudzoza kopatulika.

  • Esitere 2:12
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 12 Mtsikana aliyense ankakhala ndi nthawi yake yokaonekera kwa Mfumu Ahasiwero akamaliza kumuchitira zonse zimene amayenera kuwachitira akazi pa miyezi 12. Atsikanawo ankawapaka mafuta a mule*+ miyezi 6 kenako nʼkuwapakanso mafuta a basamu+ pamodzi ndi mafuta enanso okongoletsa miyezi inanso 6. Akachita zimenezi ankakhala kuti amaliza dongosolo lonse lowakongoletsera.

  • Salimo 45:8
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    •  8 Zovala zako zonse ndi zothiridwa mafuta onunkhira a mule, aloye ndi kasiya.*

      Umasangalala ndi nyimbo zoimbidwa ndi zipangizo za zingwe, kuchokera mʼchinyumba chachikulu cha mfumu, chokongoletsedwa ndi minyanga ya njovu.

  • Nyimbo ya Solomo 4:6
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    •  6 “Mpaka kunja kutayamba kuwomba kamphepo kayaziyazi ndiponso mpaka mithunzi itachoka,

      Ndipita kuphiri la mule

      Ndiponso kuzitunda za lubani.”+

  • Nyimbo ya Solomo 5:13
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 13 Masaya ake ali ngati bedi la maluwa onunkhira,+

      Ndiponso ngati munda wa zitsamba zonunkhira umene uli pamalo okwera.

      Milomo yake ili ngati maluwa amene akuchucha mafuta a mule.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena