21 “Bweretsani kuno mlandu wanu,” akutero Yehova.
“Fotokozani mfundo zanu,” ikutero Mfumu ya Yakobo.
22 “Tipatseni umboni ndipo mutiuze zinthu zimene zidzachitike.
Tiuzeni zokhudza zinthu zakale,
Kuti tiziganizire mozama nʼkudziwa tsogolo lake.
Kapena mutiuze zinthu zimene zikubwera.+