45 Izi ndi zimene Yehova akunena kwa wodzozedwa wake, kwa Koresi,+
Amene wamugwira dzanja lake lamanja+
Kuti agonjetse mitundu ya anthu pamaso pake,+
Kuti alande zida zankhondo za mafumu,
Kuti amutsegulire zitseko zokhala ziwiriziwiri,
Kuti mageti adzakhale osatseka. Iye wamuuza kuti:
Ndidzaphwanyaphwanya zitseko zakopa,
Ndipo ndidzadula zitsulo zotsekera zitseko.+