6 Inu nokha ndinu Yehova.+ Munapanga kumwamba, ngakhalenso kumwamba kwa kumwamba ndi magulu ake onse. Munapanganso dziko lapansi ndi zonse zili mmenemo komanso nyanja ndi zonse zomwe zili mmenemo. Mumasunga zinthu zamoyo ndipo magulu akumwamba amakugwadirani.