10 “Inu ndinu mboni zanga,”+ akutero Yehova,
“Inde, mtumiki wanga amene ndamusankha,+
Kuti mundidziwe ndi kundikhulupirira,
Komanso kuti mumvetse kuti ine sindimasintha.+
Ine ndisanakhaleko kunalibe Mulungu amene anapangidwa,
Ndipo pambuyo panga palibenso wina.+