2 Kenako Mulungu anauza munthu amene anavala zovala zansalu uja+ kuti: “Pita pakati pa mawilo,+ pansi pa akerubi. Ukatengepo makala amoto+ odzaza manja ako onse awiri kuchokera pakati pa akerubiwo, ndipo ukawaponye pamzindawo.”+ Choncho iye anapitadi ine ndikuona.