3 Anayenda mʼnjira ya mafumu a Isiraeli+ ndipo anafika mpaka potentha* pamoto mwana wake wamwamuna,+ potsatira zinthu zonyansa zimene anthu a mitundu ina ankachita+ amene Yehova anawathamangitsa pamaso pa Aisiraeli.
31 Iwo amanga malo okwera ku Tofeti, mʼChigwa cha Mwana wa Hinomu,*+ kuti aziwotcha ana awo aamuna ndi ana awo aakazi pamoto,+ chinthu chimene sindinawalamule kuti azichita ndiponso chimene sindinachiganizirepo mumtima mwanga.’*+