-
Yesaya 42:24, 25Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
24 Ndi ndani wachititsa kuti Yakobo alandidwe katundu wake
Ndiponso kupereka Isiraeli kwa anthu olanda?
Kodi si Yehova amene iwo amuchimwira?
25 Choncho Mulungu anapitiriza kuwakhuthulira ukali ndi mkwiyo wake,
Anawabweretsera nkhondo yoopsa.+
Moto unapsereza chilichonse chimene anali nacho, koma iwo sanalabadire.+
Motowo unapitiriza kuwawotcha koma iwo sizinawakhudze.+
-