-
Yesaya 66:3Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
3 Munthu amene akupha ngʼombe yamphongo ali ngati amene akupha munthu.+
Amene akupereka nsembe ya nkhosa ali ngati amene akuthyola khosi la galu.+
Munthu amene akupereka mphatso ali ngati amene akupereka magazi a nkhumba.+
Amene akupereka nsembe yachikumbutso ya lubani+ ali ngati munthu amene akupereka dalitso pogwiritsa ntchito mawu onenerera zamatsenga.*+
Anthuwo asankha njira zawozawo,
Ndipo amasangalala ndi zinthu zonyansa.
-