-
Ezekieli 18:7, 8Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
7 Sazunza munthu aliyense+ koma amabweza chikole kwa munthu amene anakongola zinthu zake.+ Salanda zinthu za ena mwauchifwamba+ koma amapereka chakudya chake kwa munthu amene ali ndi njala+ ndiponso amaphimba munthu wamaliseche ndi chovala.+ 8 Iye sauza anthu kuti amupatse chiwongoladzanja akabwereketsa zinthu ndipo sakongoza zinthu mwa katapira+ koma amapewa kuchita zinthu mopanda chilungamo.+ Iye amatsatira chilungamo chenicheni akamaweruza munthu ndi mnzake.+
-