-
Yesaya 34:5, 6Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
5 “Chifukwa lupanga langa lidzakhala magazi okhaokha kumwambako.+
Lupangalo lidzatsikira pa Edomu kuti lipereke chiweruzo,+
Lidzatsikira pa anthu amene ndikufuna kuwawononga.
6 Yehova ali ndi lupanga. Lupangalo lidzakhala magazi okhaokha.
Lidzakhala mafuta okhaokha,+
Lidzakhala ndi magazi a nkhosa zamphongo zingʼonozingʼono komanso a mbuzi,
Lidzakhala ndi mafuta a impso za nkhosa zamphongo.
Chifukwa Yehova adzapereka nsembe ku Bozira,
Adzapha nyama zambiri mʼdziko la Edomu.+
-