-
2 Mafumu 17:16, 17Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
16 Anasiya malamulo onse a Yehova Mulungu wawo nʼkupanga zifaniziro ziwiri zachitsulo za ana a ngʼombe+ komanso mzati wopatulika.*+ Anayamba kugwadira gulu lonse la zinthu zakuthambo+ ndiponso kulambira Baala.+ 17 Komanso iwo ankawotcha* pamoto ana awo aamuna ndi aakazi,+ kulosera+ ndiponso kuwombeza. Anatsimikiza mtima kuchita zoipa pamaso pa Yehova nʼcholinga chomukwiyitsa.
-