12 Koma olungama zinthu zidzawayendera bwino ngati mtengo wa kanjedza
Ndipo adzakula kwambiri ngati mtengo wa mkungudza wa ku Lebanoni.+
13 Iwo anadzalidwa mʼnyumba ya Yehova,
Zinthu zikuwayendera bwino mʼmabwalo a Mulungu wathu.+
14 Ngakhale atakalamba zinthu zidzapitirizabe kuwayendera bwino.+
Adzakhalabe amphamvu ndi athanzi,+