30Hezekiya anatumiza uthenga kwa Aisiraeli+ ndi Ayuda onse ndipo analembera makalata anthu a ku Efuraimu ndi ku Manase+ kuti abwere kunyumba ya Yehova ku Yerusalemu kudzachitira Pasika Yehova Mulungu wa Isiraeli.+
10 Choncho asilikali othamangawo anapita mʼmizinda yonse mʼdera la Efuraimu ndi Manase+ mpaka ku Zebuloni. Koma anthuwo ankangowanyoza ndiponso kuwaseka.+