Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • 2 Mbiri 33:10
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 10 Yehova anapitiriza kulankhula ndi Manase ndiponso anthu ake, koma iwo sanamvere.+

  • 2 Mbiri 36:15, 16
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 15 Yehova Mulungu wa makolo awo anapitiriza kuwachenjeza kudzera mwa atumiki ake. Ankawachenjeza mobwerezabwereza chifukwa ankamvera chisoni anthu akewo ndiponso malo ake okhala. 16 Koma iwo anapitiriza kunyoza atumiki a Mulungu woona,+ kunyoza mawu ake+ ndiponso kuseka aneneri ake.+ Iwo anafika poti panalibenso chiyembekezo choti angathe kuchiritsidwa. Kenako Yehova anawakwiyira kwambiri nʼkuwalanga.+

  • Nehemiya 9:29
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 29 Ngakhale kuti munkawachenjeza kuti ayambenso kutsatira Chilamulo chanu, iwo ankadzikuza ndipo ankakana malamulo anu.+ Iwo anachimwa chifukwa sankatsatira ziweruzo zanu zimene munthu akamazitsatira amakhala ndi moyo.+ Anatseka makutu awo ndi kuumitsa makosi awo ndipo anakana kumvera.

  • Yeremiya 7:13
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 13 Koma inu munapitiriza kuchita zinthu zonsezi,’ akutero Yehova, ‘ndipo ngakhale kuti ndinkalankhula nanu mobwerezabwereza,* inu simunamvere.+ Ndinapitiriza kukuitanani koma inu simunayankhe.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena